Prezidenti Dr Lazarus Chakwera wafika ku Rome m’dziko la Italy komwe akuyembekezeka kugwila ntchito za boma ku Vatican komanso mu mzinda wa Rome.
Pofika pa bwalo la ndege la asilikali ku Rome, Dr Chakwera pamodzi ndi Madam Monica Chakwera, analandiridwa ndi mkulu owona zinthu zochitikachitika ku Vatican, Monsignor Javier Fernandez, kazembe wa dziko la Malawi ku Vatican, a Joseph Mpinganjira, komanso kazembe wa dziko la Malawi ku Italy Dr Naomi Ngwira, mwa ena.
Dr Chakwera ali ku Italy ataitanidwa ndi mtsogoleri wa mpingo wa akatolika pa dziko lonse Papa Francis yemwenso ndi mkulu wa mzinda wa Vatican.
Poonjezera zokambirana ndi Papa Francis, mtsogoleriyu akambirananso ndi mkulu wa bungwe la St Egidio lomwe ndi la dziko la Italy pa dziko lonse komanso bungwe loona zachakudya la Food and Agriculture Organisation FAO, mwa zina.