Apolisi ku Mulanje amanga Shadreck Medson wazaka 22 pomuganizira kuti waba mbendera zadziko zokwana zisanu ndi imodzi – 6 kwa Nkhonya m’boma la Mulanje.
Ofalitsankhani zapolisi ku chigawo cha kummwera, a Edward Kabango, wati pakadali pano, apolisi akufufuza anthu ena awiri amene akuwaganizira kuti anaba nawo mbenderazo.
Malinga ndi a Kabango, anthuwo anaba mbenderazo, zomwe zinayikidwa m’mbali mwa msewu wopita ku bwalo la zamasewero la Mulanje Park kumene kunali mwambo wokumbukira anthu omwe anamwalira kamba ka namondwe wa Freddy.
Mwambowo utatha, atatuwo anapita kukaba mbenderazo limodzi ndi mitengo yomwe kunamangidwa mbenderazo, zomwe ndi za ndalama pafupifupi K540,000.
Medson ndi wa mmudzi wa Ngutuma, mfumu yaikulu Chikumbu m’boma la Mulanje.