Bungwe la Clean Cities Project pamodzi ndi khonsolo ya mzinda wa Lilongwe m’mawa uno likuyenda ulendo wa ndawala umene akutola zinyalala ndi kulimbikitsa anthu kuti adzikhala a ukhondo mu mzindawu.
Martin Manyozo, amene ali mkulu wa bungweli, wati ulendo umenewu ndi ofunikira kwambiri chifukwa uthandiza mzinda wa Lilongwe kuchepetsa chiopsyezo cha matenda a Cholera.
“Chidwi chathu chili pofuna kupereka uthenga koma tikudziwa kuti uthenga paokha siokwanira koma tichitepo kanthu nkuona tikusesa nkutoleranso zinyalala,” anatero a Manyozo.
Ntchitoyi akuyigwira mothandizidwa ndi bungwe la Waste Management komanso ma bungwe ena osiyanasiyana ku phatikizapo a European union, New restoration plan Malawi komanso Waste advisors.
Olemba ndi Kujambula: Paul Mlowoka ndi Margaret Mapando