Mafumu andodo, pansi pa bungwe lawo la Chewa Heritage Foundation (CHEFO), ati udindo waukulu wa bungwelo ndi kupititsa patsogolo, kuteteza ndi kusunga chikhalidwe ndi miyambo ya a Chewa m’dziko muno.
Izi ananena izi pamsonkhano wa olembankhani ku Lilongwe kumene anati mawu omwe mtsogoleri wa chipani cha AFORD, a Enoch Chihana, anayankhula posachedwapa zinanyozetsa komanso kupeputsa mtundu wawo.
Mfumu Chadza ati a Chihana abwere poyera kudzapepesa aChewa pasanapite masiku atatu, kuchokera lero, ndipo palibe chimene adzalipire.
Ndipo Mfumu Mwase, imene inati a Chihana ndi mdzukulu wawo, yati iyesetsa kuti ayankhule nawo kuti apepesedi.
Mafumu andodo 22 ochokera mbali zonse za dziko lino ndi amene amayenera kuti akhalepo pa msonkhanowu koma 15 ndi amene anafika ndipo ena mwa iwo ndi a Nthache, Mwase, Govati, Nthondo, Dambe, Gogo Salima ndi Masambankhunda, malinga ndi wapampando wa bungweli, a Stanley Khaila.
“A Chewa tipitiriza kukhala mwa mtendere ndi kulemekeza anthu onse a mitundu ina. Tikupempha a Malawi onse kuti tisalore kupatsa udindo anthu omwe amalimbikitsa kusankhana mitundu komanso omwe salemekeza anthu amitundu ina,” a Khaila anatero.