Mlembi wamkulu wa chipani cha Malawi Congress, a Richard Chimwendo Banda, atsimikizira anthu aku Nkhotakota kuti boma lilambula msewu wa pakati pa Mwansambo m’bomalo ndi Mponela ku Dowa podzera kwa Kasakula ku Ntchisi.
A Chimwendo Banda alankhula izi pamsonkhano omwe anakonza m’boma la Nkhotakota pamodzi ndi wapampando wa chipani cha MCP mchigawo cha Lakeshore, a Augustine Chidzanja komanso akuluakulu ena a chipanichi.
“Boma likudziwa kuti msewu umenewu ndi ofunika ponyamula mbewu za alimi kupita ku msika ndiye tiwukonza posachedwapa,” anatero a Chimwendo Banda.
Iwo ati boma lifikitsa madzi pa sukulu ya sekondale ya Mwansambo ndi kukonza zinthu zoonongeka pa chipatala cha Mwansambo.
Senior Chief Mwansambo inayamika boma chifukwa chokonza msewu wa M5 patapita zaka zambiri maboma ena atawunyozera.
“Ndi bwino kumayamika, pa zaka zinayizi bomali layesetsa kutipatsa ntchito za chitukuko komanso zosamalira anthu monga ngongole ya NEEF ndi Mtukula Pakhomo,” anatero Senior Chief Mwansambo.
Mmau ake, oyimba Skeffa Chimoto watsimikizira anthu a mderalo kuti akamusankha, awatumikira moona mtima pa chitukuko.
Ndipo a Overstone Kondowe anayamika boma chifukwa chokhwimitsa chitetezo cha anthu achi alubino, omwe anati panopa sakukhala mocheukacheuka.
Olemba: Isaac Jali