Mtsogoleri wa dziko lino Dr Lazarus Chakwera wati boma likuyika maziko okhazikika oti apindulire dziko lino kuyambira panopa mpakana mibadwo yamtsogolo.
Dr Chakwera amayankhula izi pa Kabwinja, kuzambwe kwa boma la Dowa, pamene amalankhula ndi a Malawi.
Iwo anati ngakhale dziko lino lakumana ndi ziphinjo zambiri, makamaka ngozi zogwa mwadzidzi muzaka zinayi zapitazi, zinthu zikuyenda kumbali ya ntchito zomangamanga monga misewu, nyumba za anthu ogwira ntchito ku nthambi zachitetezo ndi sukulu.
Mtsogoleriyu anati boma lionjezera chiwerengero cha opindula ku thandizo la chakudya komanso fetereza ndi mbewu zotsika mtengo kaamba kakuti limamvera zofuna za a Malawi.
Iwo anaonjezeranso kuti misewu ya kumidzi ailambula kuti alimi adzitumiza mbewu ku misika mosavuta.
Mfumu Chakhaza yaderalo inayamika boma chifukwa cha ulimi wa nthilira umene ukuchutika mderalo pa mahekitala 483, komanso chifukwa chofikitsa magetsi ndi netiweki ya lamya za mmanja.
Olemba: Isaac Jali