Malawi Broadcasting Corporation
Education Nkhani

Boma layamikira ntchito za NASCENT Solutions polimbikitsa maphunziro

Unduna zamaphunziro wayamikira bungwe la Nascent Solutions kaamba kantchito yolimbikitsa maphunziro a nkomba phala msukulu komanso a sukulu ya kwacha m’dziko muno mu zaka zisanu zomwe yakhala ikugwira ntchito mu sukulu zoposa 80.

Mlembi wa mu unduna wa zamaphunziro, a Rachel Chimbwete Phiri anena izi munzinda wa Lilongwe pomwe bungwe la Nascent Solutions limapereka kauniuni wa zotsatira zammene ntchito ya zaka zisanu yolimbikitsa kuti ophunzira msukulu akhale ndi thanzi labwino powapatsa chakudya, kotukula maphunziro a mkomba phala komanso za kwacha maboma asanu ndi limodzi yayendera.

Phiri ati ndizonyaditsa kuti kudzera muntchitoyo chiwerengero cha ana msukulu chakwera m’maboma asanu ndi limodzi kuchoka pa 54,000 kufika pa 80,000, aphunzitsi apeza luso lina pamaphunziro awo komanso makolo apeza maphunziro a kwacha kuti adziwe kuwerenga mwa zina.

M’modzi mwa akuluakulu ku Nascent Solution, a Robert Chizimba ati kauniuni wawo waonetsa kuti chiwerengero cha ophunzira chakwera maboma omwe amagwira mpaka ophunzira kusowa malo ophunziliramo ndipo ntchitoyi itha mwezi uno.

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

163,000 candidates to write JCE this year

Chisomo Break

BJ apereka uthenga wa chiyembekezo ku Chiradzulu

MBC Online

Dr Usi ali ku khonsolo ya Thyolo

Blessings Kanache
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.