Ofesi yoona za chisamaliro cha anthu munzinda wa Lilongwe yati dziko la Malawi likhoza kudzakhala ndi m’badwo wa anthu amene sadzidzakwanitsa kupereka chisamaliro choyenera kwa ana awo mu zaka 20 zikubwerazo.
Mkulu wa ofesiyi, a Derrick Mwenda, ati izi zikhoza kukhala chomwechi ngati ana amene akukula pano sakulandira chisamaliro chokwanira chochokera kwa makolo onse.
A Mwenda amalankhula izi mu mnzindawu pa zokambirana zimene bungwe la SOS Children’s Villages linakonza zolimbikitsa kuti ana adzikula m’mabanja oyenera mmene muli makolo onse.
Iwo anapempha mabungwe osiyanasiyana kuti athandize boma kulimbikitsa mabanja kuti adzikhala odzidalira paokha ndi kumasamalira ana awo.