Kuvumba mabindula madzulo ano pa Kamuzu Institute of Sports pakati pa ziphona zazigogodo ziwiri Limbani Masamba komanso Simeon Tcheta pa nkhonya yolimbirana lamba yomwe yakonzedwa ndi a New Dawn Boxing Promotion.
Mphongozi zakhala zikuyankhula mopeputsana ndipo zinatsala pang’ono kuyamba kuponyerana zibakera loweluka pa 1 June 2924, pomwe zimakwera sikelo panja pa Kamuzu Institute.
Masamba wauza Tcheta kuti aona mbwadza chifukwa ali ndi mkwiyo ndi zomwe zinachitika chaka chatha pomwe iye anagonja pa ma points ndi Tcheta.
“Ndikubwera kudzabweza chipongwe ndipo ukonzeke chifukwa ndidzakupanga zoopsa ulendo uno, ” walavula moto chotere Masamba pomwe Tcheta watemetsa nkhwangwa pamwala kuti malodzawa amuonekera yekha Masamba chifukwa ulendo uno sakamaliza nkhonyayi pomwe akamugwetse ndiija amati “Knock out.”Mkulu wa kampani ya New Dawn Boxing, a Mike Chimaliza, ati kwaiwo ntchito yawo achita kwatsala ndikwa anyamatawa kuti akafotokoze bwino za zomwe akhala akuyankhulanazi masana ano.
Anyamatawa anamenyanapo pa M1 Center Point chaka chatha m’mwezi wa May ndipo Tcheta anagonjetsa Masamba kudzera pa ma points zomwe Masamba anati sanamvetse ndipo anapempha kuti akumanenso.