Akuluakulu apa chipatala chachikulu cha Mzuzu ati chipatalachi chikulandira abambo pafupifupi 60 mwezi uli ofuna chithandizo cha nthenda ya khansa ya chida cha abambo, penile cancer mchingerezi.
Malinga ndi Dr Alex Khombedza yemwe amayang’anira ntchito zamdulidwe pa chipatalachi, ambiri mwa abambowa ndi ochokera mzipatala zosiyanasiyana m’chigawo chakumpoto ndipo amafika zinthu zitaonongeka kale kaamba koti nthendayi imayamba ndi timatuza tomwe timanka tikula kutsogolo kwa chida cha abambo.

Pa tsiku, chipatalachi chimalandira odwala matendawa awiri kapena atatu ndipo Dr Khombedza ati mdulidwe ndi njira yomwe ingathandize polimbana ndi vutoli.
Iwo amalankhula pamaphunziro a olembankhani m’chigawo chakumpoto amene anakonza ndi bungwe la JournAids linakonza ku Mzuzu.

Pakanali pano katswiri pa nkhani za umoyo George Jobe wati mpofunika kuti ma uthenga okhudza nthendayi afikile pali ponse pofuna kuteteza abambo ambiri ku nthendayi.