Mnyamata wadzigogodo wamdziko muno,Mussa Ajibu, lero wagonjetsa mnyamata wamtali ochokera m’dziko la South Africa, Ruan Vissah pamasewero ankhonya amene anachitikira munzinda wa Lilongwe.
Majaji onse atatu anati Ajibu ndiye wachita chamuna pamasewerowo potibula mnzakeyo.
M’masewero ena komweko, Alick Mwenda wadziko lino nayenso zake zayenda atagonjetsa Trancy Ntetu ochokera m’dziko la Canada pakutha pa ma round asanu ndi imodzi.