Malawi Broadcasting Corporation
Local Local News Nkhani

Amayi a Zokonda Amayi apulumuka pangozi

Gulu la amayi a Zokonda Amayi a m’chigawo chakummwera lapulumuka pa ngozi ya bus imene yachitika m’boma la Ntcheu usiku wa Lachitatu.

Amayiwa amachokera munzinda wa Mzuzu kumene anali nawo pa mwambo wa chaka chino wa Zokonda Amayi Macheza.

Mlembi wa Zokonda Amayi Blantyre Chapter, a Catherine Sankhula Banda, ati ngoziyi yachitika atatsala pang’ono kufika pa Salima Turn-Off pamalo otchedwa Chisoni pamene bus imene anakwerayo imalephera kukwera mtunda.

Koma a Banda anatsutsa zimene zikumveka m’masamba amchezo kuti amayi ambiri avulala modetsa nkhawa.

Ofalitsankhani ku nyumba yowulutsa mawu ya boma ya MBC, a Chisomo Mwamadi, ati eni ake a galimotoyi, a Ulemu Bus Service, atumiza bus ina kuti ikawatenge amayiwa.

Iwo atinso amayi 16 ndi amene anathamangira nawo ku chipatala koma sanawagoneke.

Olemba: Chipiliro Mtumodzi

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

‘Anthu achikulire akhale ndi mwayi ovota’

MBC Online

Dr Chakwera ayamikira anthu ku Nsanje posamukira kumtunda

MBC Online

Immigration starts clears out passports backlog at LL office

Mayeso Chikhadzula
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.