Apolisi ku Mangochi amanga amai atatu powaganizila kuti anaba zigubu za oilo wa galimoto mu sitolo ya Chipiku.
Ofalitsa nkhani za polisi ya Mangochi, a Amina Tepani Daudi, auza MBC kuti amaiwa ndi a Diana Thukuwa azaka 60, a Rose Samson azaka 66 komanso ndi a Lucy Mangani azaka 64.
“Malipoti omwe tili nawo ndi okuti pa 2 January chaka cha 2025 amai atatuwa analowa mu sitoloyi ndikuba katunduyu koma mmodzi mwa ogwira ntchito mu sitoloyi ndi amene anawazindikira kuti atulutsa katundu mokuba,” atero a Daudi.
Iwo atinso malipoti apolisi akuonetsanso kuti a Thukuwa adakhalapo ku ndende zaka ziwiri pamulandu ngati omwewu pamene a Samson adawamanga mwezi watha atawagwira atabanso mu sitolo ina yogulitsa katundu osiyanasiyana.
Atatuwa akaonekera kubwalo lamilandu kukayankha mulandu okuba.