Bungwe lopereka ngongole la National Economic Empowerment Fund (NEEF) lagawa feteleza wangongole kwa alimi am’magulu komanso oima pawokha mdera la mfumu yaikulu Chimutu mboma la Lilongwe.
Poyankhula pamwambo opeleka fetelezayu, mkulu wa bungwe la NEEF, a Humphrey Mdyetseni, ati cholinga cha ntchitoyi ndikuonesesa kuti alimi m’dziko muno akupeza mwayi wa feteleza yemwe awathandize kupeza zokolola zochuluka chaka chino.
A Mdyetseni anatiso Iwo ngati bungwe akuyembekezera kulandira ndalama zoonjezela ku boma kuti afikile alimi ena omwe akusowa fetelezayu.
Phungu wadelari a Winston Kayipanjila apempha alimi omwe apindula ndi ngongole ya fetelezayu kuti amugwilise ntchito moyenela ndicholinga choti azapeze zokolola zochuluka zomwe zizawathandize kubweza ngongoleyi komanso kupeza mwayi otenga ngongole ya feteleza wina.
Kumbali yawo a senior group ntchoka anayamikila bungwe la NEEF kaamba kangongoleyi yomwe iwo ati ipindulira alimi ochuluka mdelari omwe sangakwanise pawokha kugula fetelezayu.
Bungwe la NEEF lakhala likuyenda madela osiyanasiyana kupereka feteleza wangongoleyi yemwe akuyembekezera kupindulira alimi pafupifupi 400,000.
Olemba: Emmanuel Chimutu