Nduna yoona za madzi, a Abida Mia, ati ndi okondwa ndi kulimbikira kwa anthu a m’dera la Chikwawa Nkombezi, kumenenso iwo ndi phungu wawo.
A Mia anayendera alimi a kwa Nsomo, amene ali pansi pa Mikalango EPA m’dera la mfumu Ngabu.
Kumeneku akuwetako zifuyo zambiri zimene ndowe zake akupangira manyowa ndi kugwiritsa ntchito ku minda ya mnthilira pa sikimu ya Mthiransembe.
“Tangoonani, ma bedi a anyezi onsewa. Pa bedi imodzi akupeza K400,000. Palinso mbewu zambiri, si kutukuka kumeneku?” anafunsa a Mia.
Iwo ati athandiza alimiwa powalumikizitsa ku ndondomeko yobwereka ndalama ya NEEF komanso awathandiza ndi ndalama zokonzetsera mapampu amene anaonongeka ndi cholinga chakuti achulutse zokolola zawo.