A Chikosa Silungwe, omwe anali nzawo wa malemu Dr Saulos Chilima, ati malemu Dr Chilima anathandiza kumenyera kuti m’dziko muno mubwere ulamuliro wa zipani zambiri (multiparty democracy).
A Silungwe ati Dr. Chilima anapanga zimenezi mogwirizana ndi anzawo ambiri amene pa nthawiyo anali msukulu zosiyanasiyana za ukachenjede.
A Silungwe atinso Dr. Chilima anali munthu wa nzeru, wamsangala kwambiri ndipo kuli konse komwe adagwira ntchito amasiya mbiri yabwino.
Pothilira ndemanga pa ntchito za boma, iwo anati Dr. Chilima amaonetsa chitsanzo monga kusunga nthawi komanso kudzipereka kwathunthu pogwira ntchito iliyonse.
A Silungwe agwirizana ndi akubanja la a Chilima kupempha boma kuti pachitike kafukufuku wokwanira pa ngozi imene yadzetsa imfayi.
Olemba: Isaac Jali