Bungwe lolimbana ndi ziphuphu komanso katangale la ACB lasayinirana mgwirizano ndi nthambi yoona zotuluka komanso kulowa m’dziko muno ya Immigration kuti agwilire ntchito limodzi polimbana ndi ziphuphu komanso katangale.
Izi zikudza patangotha sabata imodzi kuchoka pamene ACB inamanga anthu ena ogwira ku immigration munzinda wa Lilongwe kaamba kowaganizira kuti akukhudzidwa ndi mchitidwe waziphuphu.
Poyankhula munzinda wa Lilongwe, ogwirizira udindo wamkulu wa ACB, a Hillary Chilomba, ati mgwirizano wa zaka zinayiwu sikuti ujejemetsa magwiridwe antchito a bungwe lawo pa anthu amene anawamangawo koma kuti tsopano ziwapatsa mangolomera kuti apitirize ntchito yoonetsetsa kuti anthu akutumikiridwa bwino ku nthambi ya Immigration.
M’modzi mwa ma komishonala ku Immigration, a Fletcher Nyirenda, ati nawo ndiokondwa ndi mgwirizano umene asainirawu kuti athetse mchitidwe waziphuphu pamodzi ndi bungwe la ACB.
Olemba: Austin Fukula