Nduna yoona zamaphunziro apamwamba, a Jessie Kabwila, yati boma likulimbikitsa aliyense amene akufuna kupeza mwayi wangongole ku bungwe la National Economic Empowerment Fund (NEEF) kuti akatenge.
Ndunayi imayankhula izi m’boma la Mangochi pamene imayendera sukulu ina imene mwini wake adamanga kudzera ku ngongole ya NEEF.
“Mu uthenga wake opita ku mtundu wa a Malawi, mtsogoleri wadziko lino, Dr Lazarus Chakwera, adati pali zambiri zimene wachita kudzera kubungwe la NEEF ndipo chimodzi mwaicho ndi sukulu yomwe mukuyionayi, izi zikutanthauza kuti Dr Chakwera wakangalika kutukula maphunziro m’boma lino,” a Kabwira anatero.
Mwini sukuluyi, a Winston Majamanda, anati ngongole ya NEEF ndi yopindulitsa kwa munthu amene alibe mantha aliwonse pachinthu chimene akufuna kuchita.
“Panopa ngongole yomwe ndidatenga ndinamaliza kubweza ndipo ndikukatenganso ina kuti ndimange sukulu ya pulayimale,” a Majamanda anatero.
Mmodzi mwa akuluakulu a NEEF, a Harmony Mwavuli, anati NEEF imafuna chikole ngati njila imodzi yakuti obwereka ndalamayo adzikumbukira kubweza pang’ono pang’ono.
Komabe, a Mwavuli anati ichi sichinthu chokanikitsa munthu kukatenga ngongole ku bungwelo chifukwa kulinso ngongole zina zosafunikira chikole monga ngongole imene amayitcha ‘Vuwukani’.