Timu ya Silver Strikers yati K6 million imene FCB Nyasa Big Bullets yapereka ndi yosakwanira kukonzetsera bus yawo imene idaphwanyidwa pa ziwawa zomwe zidachitika ku Blantyre nthawi imene matimuwa amasewera.
Mkulu wa timuyi, a Patrick Chimimba, ati pakufunika ndalama zoposa K10 million kuti akonzetsere galimoto yawo.
“Ma koteshoni atatu ndi andalama zosachepera K10 miliyoni kwacha koma tinavomera k6 miliyoni kamba kakudzichepetsa kwawo chifukwa nkhani siyolanga bullets,” anatero a Chimimba.
Koma a Chimimba ayamikira timu ya Bullets popereka K6 million kaamba kovomereza kulakwa kwawo.
“Ndizosowa, nde kwatsalako tichita ndi ifeyo,” iwo anatero.

Iwo analangizanso otsatira matimuwa kuti adzitha kuvomereza zotsatira zilizonse pa masewero a mpira wa miyendo komanso kupewa ziwawa.