Bwalo la Senior Grade Magistrate ku Blantyre lachiwiri lapeza olakwa abambo awiri komanso kuwalanda belo chifukwa chopalamula milandu yozembetsa zinthu zamu nkhalango yotetezeka.
Amuna awiriwa omwe ndi a Jonasi Billiat ndi Evison Michael akuyankha milandu yozembetsa zinthu zamu nkhalango ya boma komanso kupezeka ndi zinthuzo popanda zikalata zachilolezo.
Malinga ndi omwe atsina khutu MBC Digital amuna awiriwa mwezi wa December m’chaka cha 2023 adawagwira ndi matumba 205 amakhala pamalo wochitila chipikisheni apolisi a GDC roadblock mbandakucha.
Poyankhula mbwaloli wapolisi woimila boma pa mlandu, Levison Mangani anati sikoyamba a Billiat kupezeka ndi mlandu otere.
Iwo anauza bwaloli kuti mwezi wa April mchaka cha 2021 abambowa adawapezanso olakwa pamlandu ngati omwewu ndipo adapeleka chindapusa cha K200,000 ndipo galimoto zawo ziwiri adaziombola ndi ndalama zokwana K400,000.
Wapolisi woimila bomayi anapemphanso kuti galimoto zomwe anagwilitsa ntchito popalamula mlanduwu azilande kaamba koti zikuthandizila kupalamula mlandu.
Pakadali pano, Senior Grade Magistrate M’manga akuyembekezeka kupeleka chigamulo pamlanduwu Lachisanu pa 17 January 2025.