Alimi ang’ono ang’ono olima mpunga omwe amagwilira ntchito mmagulu kwa Maganga m’boma la Salima akuyembekezera kupha makwacha ndi ulimi wamakono wa mpunga kutsatira kuchita bwino kwa mbewu yawo kudzera mu upangiri wa bungwe la African Institute of Corporate Citizenship (AICC).
Alimiwa ati akusiyanitsa phindu lomwe akupeza chiyambileni ulimi wamakonowu kaamba kakuti mbewu yawo ikuchita bwino ngakhale ambiri akhudzidwa ndi mavuto a kusintha kwa nyengo.
Bungwe la AICC limapereka maphunziro akalimidwe ka makono ndi luso pofuna kuti alimi apeze phindu lochuluka pa zolima zawo.
Mkulu wa bungweli, a Driana Lwanda, wati ulimi wampunga wamakono ndi opindulitsa chifukwa umasungira madzi amene amathandiza mbewu kuchita bwino posatengera mavuto odza kaamba ka kusintha kwa nyengo monga ng’amba.
Bungwe la AICC likugwira ntchitoyi ndi thandizo la ndalama lochokera ku bungwe la We Effect.