Apolisi kwa Namalaka m’boma la Mangochi amanga Mofolo Yohane,22, yemwe ndi msodzi pomuganizira kuti anakhapa m’mutu Bashir Haji, wa zaka 13, ndi cholinga chakuti amuphe ndi kukhwimira malonda ake ogulitsa nsomba.
Ofalitsa nkhani za Polisi ya Mangochi, a Amina Tepani Daudi, atsimikiza nkhaniyi ndipo ati Mofolo akaonekera ku bwalo lamilandu kukayankha mulandu ofuna kupha.
“Titamufunsa Mofolo ananena kuti anawuzidwa ndi sing’anga kuti apititse zikope za munthu wakufa komanso madzi osambitsira maliro kuti bizinezi yake ipite patsogolo,” a Daudi anatero.
Yohane amachokera m’mudzi mwa William kwa mfumu yaikulu Nankumba ku Mangochi.