Mtsogoleri wa dziko lino, Dr Lazarus Chakwera, lero akhala nawo pa mwambo wa mapemphero pa mpingo wa Monkey Bay Assemblies of God m’boma la Mangochi.
Mwambo wa mapemphero umenewu ukuyembekezeka kuyamba nthawi ya 9 koloko m’mawa uno.
President Chakwera ali m’chigawo chaku m’mawa kumene akugwira ntchito zaboma.
Olemba: Owen Mavula