Malawi Broadcasting Corporation
Nkhani

Prezident Chakwera wafika pa Kaphuka Trading Centre ku Dedza

Mtsogoleri wadziko lino, Dr Lazarus Chakwera, ali kwa mfumu yayikulu Kaphuka ku Dedza pamsonkhano wakalawe m’bomali.

Polankhula kwa anthu ochuluka omwe anasonkhana pa sitolo za pa Kaphuka, Dr Chakwera anati akudziwa bwino za njala imene anthu ali nayo mderali kaamba ka ng’amba yomwe inalipo chaka chatha.

Mtsogoleriyu watsimikizira anthu kuti chakudya chomwe boma layamba kale kugawa chifika posachedwapa kuderali.

Pamenepa, iye analimbikitsa anthuwa kuti asaiwale kukalembetsa mukaundula wa chisankho kuti adzathe kuponya nawo mavoti chaka cha mawa.

Ndipo phungu wadera la Dedza Central East, a Joshua Malango, apempha boma kuti lionjezere thandizo la chakudya kuderali.

Phunguyu wapemphanso anthu mderali kuti apitirize kukalembetsa maina mukaundula wa chisankho kuti adzathe kuvota pa chisankho chaka chamawa.

Related posts

Chepetsani chinyengo poweruza milandu — Mzikamanda

Alinafe Mlamba

Awamanga powaganizira kuti amafuna kulowetsa chamba ku ndende

Romeo Umali

Fumbi koboo kumwambo wa Prison Health Day

Yamikani Simtowe
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.