Gule kuwonetsa luso lophwanya njerwa pa ndende ya Maula mumzinda wa Lilongwe.
Chindime ndi Phunkwaku komanso magulu oimba, ndi gule wamkulu wa pa ndendeyi ndi ena mwa omwe asangalatsa anthu pa mwambo womwe ukutchedwa Prison Health day.
Bungwe la National Aids Commission ndilomwe lathandiza nthambi ya ndende ya Malawi Prison Service ndi ndalama zochitira mwambo umenewu, womwe cholinga chake ndikufuna kulimbikitsa ukhondo komanso kuchepetsa kufala kwa matenda opatsirana pogonana komanso chifuwa chachikulu (TB) pakati pa akaidi ndi ena omwe akusungidwa pa ndendeyi.
Anthu oposera 3000 ndi omwe akusungidwa pa ndendeyi, yomwe imayenera kusunga anthu osaposera 1000.
#MBCDigital
#Manthu