Apolisi ku Zomba amanga Estery Evance wazaka 19 ndi Bonface Phiri wazaka 22 powaganizira kuti amafuna kulowetsa chamba ku ndende yaikulu ya Zomba.
Ofalitsankhani wapolisi ku Zomba, Patricia Sipiliano, wati Phiri, yemwe ali pa limande ku ndende ya Zomba, anakaonekera ku khoti pa mlandu womwe anapalamula m’mbuyomu.
Pomwe Phiri amabwelera ku ndende, Evance anatenga nsapato zomwe zimadziwika kuti Gwaladi ndikupereka kwa mzakeyo ndipo oyang’anira ndende anadabwa ndi izi.
Iwo atayang’ana pansi pa nsapatozo pomwe panali pong’ambika, anapeza kuti kwabisidwa fodya wamkulu. Atawafunsa, anlephera kufotokoza zomveka.