Malawi Broadcasting Corporation
Local Local News Nkhani

Boma lakhudzika ndi ngozi ya ku Kasungu

Ofalitsa nkhani za boma, a Moses Kunkuyu, ati boma ndi lokhudzidwa kwambiri ndi imfa za anthu 26 omwe amwalira pangozi ya galimoto m’boma la Kasungu lero m’mawawu.

Ngoziyi yachitika pamene minibus yomwe imachokera kwa Jenda kupita ku Lilongwe inawombana ndi galimoto lalikulu lonyamula mafuta yomwe inagundanso munthu wina yemwe amapalasa njinga zomwe zinapangitsa kuti pabuke moto woopsa.

A Kunkuyu anati mtsogoleri wa dziko lino, Dr Lazarus Chakwera pamodzi ndi mayi wa pfuko lino, Madam Monica Chakwera, ali ndi chisoni chachikulu ndi imfa ya anthuwa.

Iwo ati Dr Chakwera alamula kuti achite chilichonse chothekera popereka thandizo lofunikira mabanja onse oferedwa pa ngoziyi ndipo anati boma liwonetsetsa kuti onse atisiyawa apatsidwe ulemu woyenera.

 

Related posts

Offering hope to Cyclone Freddy victims: A year after disaster

Alinafe Mlamba

Amabera anthu powanamiza kuti amachulukitsa ndalama

Romeo Umali

MEC ENGAGES ARTISTS IN ELECTORAL PROCESSES AND REFORMS

Rabson Kondowe
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.