Apolisi ku Zomba amanga sing’anga wa ku Mozambique, Asima Abdul, pomuganizira kuti waba ndalama za mayi wina pomunamiza kuti ali ndi mankhwala ochulukitsa ndalama.
Ofalitsankhani wapolisi ku Zomba, Patricia Sipiliano, wati Abdul, yemwe ali ndi zaka 31, anauza mayi Linda Mfupika kuti amupatse ndalama zokwana K125,000 kuti azichulukitse mukanthawi kochepa.
Koma mayiyo anadabwa kuti nthawi ikudutsa ndipo ndalamazo sizikuchuluka.
Atamufunsa, sing’anga wachinyengoyo anauza mayiyo kuti azimu akana ndalamazo chifukwa zachepa ndipo awonjezere.
Apa mayi Mfupika anazindikira kuti munthuyo ndi wachinyengo ndipo anakanena ku polisi.