Malawi Broadcasting Corporation
Nkhani

Mia adzudzula mchitidwe owononga zitukuko za madzi

Nduna yoona zamadzi ndi ukhondo, a Abida Mia, yadzudzula mchitidwe owononga ma pipe a amadzi komanso kuba zipangizo zothandizira kugawa madzi m’dziko muno.

A Mia amayankhula izi mumzinda wa Lilongwe pamene anatsogolera mwambo otsekulira paipi yamadzi aulere kwa anthu aku Area 28 imene a kampani ya Sungold Food Processing Limited apereka kuti ithandize anthu mderali kupewa matenda odza kamba komwa madzi osatetezeka.

Izi zikudza pomwenso kanema wina anaonetsa amayi ena akuswa mapayipi amadzi, zomwe ndunayi yati ndi mchitidwe odzikonda.

Mkulu wakampani ya Sungold Food Processing Limited, a Mahesh Ghedia, ati iyi ndi ntchito yomwe yangoyamba ndipo mabilu onse amadziwa idzilipira ndi kampaniyi.

Phungu wadera lapakati mumzinda wa Lilongwe, a Alfred Jiya, wayamikira ntchitoyi ndipo wati udindo onse osamala ntchitoyi uli mmanja mwawo.

Ntchito yomanga makiyosiki amadzi omwe ndi otetezeka a waterboard inayamba chaka chatha.

Related posts

Timu ya Hilltop Socials yawina chikho cha under 21 ku Mzuzu

Alinafe Mlamba

Ulendo wapsya waku 2024 Paris Paralympic

Alinafe Mlamba

Azaumoyo akufufuza za imfa ya achinyamata aku Manase

Rabson Kondowe
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.