Mu chinthuzi: Gift Kawalazira – Dotolo otsogolera ntchito zaumoyo ku Blantyre
Akuluakulu oona za umoyo munzinda wa Blantyre ati akufufuza za achinyamata ena amene malipoti akusonyeza kuti amwalira atamwa mowa wina mdera la Manase mumzindawu.
Kalata imene yasayinidwa ndi dotolo otsogolera ntchito za zaumoyo ku Blantyre, a Gift Kawalazira, ikusonyeza kuti kafukufuku wa azachipatala wapeza kuti achinyamata asanu ndiwo amwalira pamene ena awiri akulandira thandizo pa chipatala chachikulu cha Queen Elizabeth atamwa mowa umene akuuganizira kuti wadwalitsa anyamata awiriwo ndinso kupha asanu enawo.
Anthu ena ati achinyamata ambiri akumakonda kumwa mowawo mma shabeen, umene ndiwaukali ndipo ena akuutchula kuti ‘mbuye tengeni’.