Mmodzi wa ounikira nkhani za utsogoleri wabwino, Undule Mwakasungula, wayamikira mtsogoleri wa dziko lino, Dr Lazarus Chakwera, pobweretsa chikhulupiliro mwa a World Bank pamene yapereka K613 billion yomangira malo opangira mphamvu za magetsi a Mpatamanga m’boma la Blantyre.
A Mwakasungula ati ntchitoyi ikadzatha idzachititsa dziko lino kukhala ndi mphamvu za magetsi zodalirika, zomwenso angadzamagulitse m’mayiko ena.
Iwo ati ma ulamuliro ena mmbuyomu akhala akusakaza ndalama zoterezi, zimene zapangitsa dziko la Malawi kukhala ndi mavuto ochuluka m’magawo osiyanasiyana.
Iwo alangiza boma kuti ndalamazi zigwire ntchito yoyenera.
Olemba: Blessings Cheleuka