Malawi Broadcasting Corporation
Development Education Local Local News Nkhani

MZUNI alumni yapereka K2.9M kwa ophunzira osowa

Ophunzira akale apa sukulu ya Mzuzu University apereka K2.9 million kwa ophunzira osowa apa sukuluyi ndicholinga chakuti iwathandizire fizi komanso zinthu zina.

Amene wayimira mkulu wa bungwe la ophunzira akalewa, a Douglas Nyirenda, ati K1.9 million ndi fizi kwa ophunzira asanu ndi m’modzi pamene K1 million ndi ya zina ndi zina kwa ophunzira asanu ndi anayi.

“Cholinga chathu ndi kuthandiza ophunzira osowa amene ali pa sukukuyi, omwe ambiri mwa iwo, afika posiya sukulu kaamba kosowa fizi ndi zina, choncho ndife odzipereka kuthandiza ophunzira,” a Nyirenda anafotokoza.

Iwo anati ophunzira ambiri pasukuluyi ali pa chiopsezo chosiyira panjira maphunziro awo kaamba kopanda fizi, chakudya komanso pogona. Kotero, iwo apempha anthu ndi mabungwe akufuna kwa bwino kuti achitepo kathu popereka thandizo losiyanasiyana.

Amene anayimira wachiwiri kwa mkulu wasukuluyi, Dr Aubrey Chaputula, anathokoza ophunzira akalewa ponena kuti chaka chili chonse ophunzira akuchoka pa sukukuyi kaamba kosowa fizi ndi zithu zambiri.

M’modzi mwa ophunzira amene walandira nawo thandizoli, amene ali mu chaka chake chomaliza, James Stewart, wati iye ndi anzake ndi okondwa komanso othokoza kaamba kakuti m’modzi mwa iwo anasiya kubwera kusukulu kaamba ka fizi.

Malinga ndi akuluakulu apa sukuluyi, mwa ophunzira 9,000 omwe anali nawo, ophunzira oposa makumi awiri amasiyira pa njira maphunziro awo teremu iliyonse.

Olemba: George Mkandawire

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Abwezedwa ndi komiti

Beatrice Mwape

US-based non-profit organisation brings health services closer to communities

Yamikani Simutowe

Muslims urged to advocate for peace and stability in Malawi

Sothini Ndazi
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.