Nthambi ya DoDMA yatsimikiza kuti ifikira anthu onse amene akhudzidwa ndi njala m’dziko muno.
M’modzi mwa akuluakulu ku nthambiyi, a Fyawupi Mwafongo, anena izi ku nkhokwe za chimanga ku Kanengo munzinda wa Lilongwe pamene amanyamula chimanga cha matani 4,000 kudzera pa stima yapamtunda, chimene akachigawe kwa anthu amene njala inawakhudza m’chigawo cha kummawa.
A Mwafongo ati DoDMA ndi yokonzeka kwambiri kuti ipereke chimanga Kwa anthu amene zovutazi zawakhudza ndipo akugwiritsa ntchito stima ya pamtunda komanso galimoto kuti akafikire anthuwa mu nthawi ya bwino.
Iwo anatinso ndi okondwa ndi kukonzedwanso kwanjanji m’dziko muno imene anati akunyamulirapo chimanga chochuluka pakamodzi ndi kufikira anthu mwa msanga komanso kupulumutsa ndalama zochuluka.