Apolisi m’dziko la America amanga a Vem Miller, 49, powaganizira kuti amafuna kupha mtsogoleri wakale wa dzikolo, a Donald Trump.
Malinga ndi ofalitsankhani wa apolisi kumeneko, a Chad Bianco, oganiziridwayu, yemwe amanamizira kuti ndi mtolankhani, anamugwira akufuna kulowa pa zipata za bwalo la Coachella Valley ku California komwe a Trump amachititsa msonkhano okopa anthu.
Apolisi atafufuza m’galimoto mwa a Miller anapezamo mfuti ziwiri, zipolopolo zochuluka komanso ziphaso zoyendera zachinyengo zomwe zinali ndi mayina a anthu osiyanasiyana.
A Miller akhala munthu wachitatu kumangidwa poganiziridwa kuti amafuna kupha a Trump.
A Trump, omwe ndi achipani chotsutsa cha Republican, ndi mmodzi mwa anthu omwe akupikisana nawo pa udindo wa mtsogoleri wa dzikolo pa zisankho zomwe zichitike mu November chaka chino.
Olemba: Alufisha Fischer