Malawi Broadcasting Corporation
Local Local News Nkhani Politics

‘Mudzatuluke mwaunjinji kukavotera Dr Chakwera’

Mlembi wa mkulu wa chipani cha Malawi Congress (MCP) a Richard Chimwendo Banda walimbikitsa anthu m’boma la Lilongwe kuti adzavotere mtsogoleri wa dziko lino Dr Lazarus Chakwera pachisankho cha pa 16 September 2025.

A Chimwendo Banda ayankhula izi Lamulungu ku khwimbi la anthu limene linasonkhana pa bwalo la Mkwinda ADMARC ku Bunda m’bomali.

Iwo ati kulembetsa mavoti ndi nkhani ina koma kuvota ndi kumene kuli kofunikira kuti Dr Chakwera apitirize ntchito yachitukuko.

Wapampando wa chipanichi m’chigawo chapakati, a Patrick Zebron Chilondola, anati kuli konse kumene akuyenda limodzi ndi a Chimwendo Banda, akulimbikitsa mtendere pakati pa anthu onse m’chipanichi pozindikira kuti izi ndi zimene zingapangitse kuti MCP ikhalebe ndi mphamvu m’madera onse.

“Inetu ndikunena kuti nkhani yogawikana inatha pomwe tinachita masankho a chipulula! ino ndi nthawi yakuti onse amene anapambana ngakhalenso kugonja pa zisankhozi tigwirane manja kuti chipani chathu chipitilire kukhalabe cha mphamvu,” a Chilondola anatero.

Iwo anaonjezeranso kuti onse amene anapambana mu chisankho cha chipulula akuyenera agwire ntchito limodzi ndi iwo amene anagonja pofuna kuti Dr Chakwera adzapambane pa chisankho chikubwerachi.

Olemba: Isaac Jali

Related posts

Woman nabbed for peddling fake HIV/AIDS cure

Rabson Kondowe

Osewera akale a Flames aimba lokoma

Rabson Kondowe

Police Officers urged to lead in child rights protection

Rabson Kondowe
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.