Malawi Broadcasting Corporation
Nkhani

Khonsolo ya mnzinda wa Zomba ili ndi Mfumu yatsopano

Khonsolo ya mnzinda wa Zomba yasankha a Christopher Jana adera la Mpira ngati mfumu yatsopano ya mnzindawu.

A Jana alowa mmalo mwa a Davie Maunde omwe akhala pa mpandowu kuchoka chaka cha 2021 atasankhidwa mmwezi wa December mchakacho.

A Anthony Gonani ndiye wachiwiri kulowa mmalo mwa a Munira Bakali a Likangala ward.

A Jana anakhalaponso pa udindowu mchaka cha 2018 kufika 2020 pomwe khansala Benson Bula anatenga udindowu kufikira 2021.

Related posts

GESD yayamba kumanga mlatho wa Limbe

Rabson Kondowe

Gwiritsani ntchito zitukuko kuti dziko lino lipindule

Alinafe Mlamba

Khulubvi Arts and Cultural Festival yafika pa mpondachimera

Rabson Kondowe
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.