Zokonzekera zokhudza phwando la maimbidwe la Ku Mingoli zayambika pa bwalo la masewero la Civo mu mzinda wa Lilongwe pamene phwandoli lichitike loweluka likubwerali.
Khonsolo ya mzindawu nayo yachita mgwirizano ndi oyendetsa phwandoli pomwe masanawa mfumu ya mzindawu a Esther Sagawa anatsogolera ntchito yosesa malo ozungulira bwaloli.
Oimba oposa 21 a m’dziko muno ndi omwe adzayimbe patsikuli kufikira m’mawa wa tsiku Lamulungu.