Kampani ya lamya za mmanja ya TNM yalengeza kuti ipereka mabandulo a chipukutamisonzi kwa makasitomala ake oposa 1million kamba kopilira ku vuto la internet limene linakula sabata yatha.
Mkulu owona za malonda ku TNM, a Sobhuza Ngwenya, ndiye wayankhula izi pa msonkhano wa atolankhani ku Blantyre.
“Sabata yatha tinali ndi vuto la internet kamba kakuduka kwa nthambo za pansi pa nyanja zomwe zinakhudza kwambiri ntchito zathu, pano takwanitsa kukonza vutoli pogwiritsa ntchito njira zina, ndipo tsopano internet yathu ili bwino kuposa kale,” watero Ngwenya.
Pakalipano, kampaniyi yati yagwiritsa ntchito K4 billion pothana ndi vutoli.
Olemba : Mercy Zamawa