Malawi Broadcasting Corporation
Uncategorized

‘Tiyamba kuchita bwino pa masewero mu 2030’

Olemba: Hassan Phiri

Mkulu oyang’anira bungwe la zamasewero la Malawi National Council of Sports, a Henry Kamata, amema mabungwe onse amene ali pansi pawo kuti achilimike kusula osewera amene adzikapambana ma mendulo osiyanasiyana ku mipikisano yakunja.

A Kamata ati chimene chikulepheletsa Malawi kuti isamachite bwino, mwazina, ndichakuti palibe ndondomeko zimene zimalondoloza osewera akayamba kuchita bwino kuti asungike nthawi yayitali ndikumuthandiza kuti achite bwino ku mipikisano monga Commonwealth, All African Games, Olympic ndi ena.

“Osewera amene anakayimilira dziko lino ku Regional Five games yaku Lesotho mchaka Cha 2021 ndi ena amene anasewera ma games aku Lilongwe, lero alikuti? Anafunsa chomwecho akamata. Iwo ati “pakufunika pakhale ndondomeko yabwino imene idzilondoloza osewera amene tikusula panopa kuti pofika chaka cha 2030 tikhale ndi timu yamphamvu ya osewera odziwa kuti akayambe kuwina ma mendulo kumipikisano yakunja.”

Iwo ati ayika ndondomeko, kuphatikizapo kuphunzitsa adindo kuti adziwe ndondomeko zabwino zosamalira osewera ndikuwasunga bwino, kulimbikitsa kuti osewera asamabere zaka komanso dziko la Malawi likhale ndi mabwalo oyenelera osewelera masewero monga Basketball, Tennis, Volleyball, ndi zina.

Bungwe la MNCS linakonza mkumanowo munzinda wa Mzuzu.

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

MBC holds corruption and fraud awareness for staff

MBC Online

ASSOCIATION OF MEDICAL COUNCILS OF AFRICA ANNUAL CAPACITY-BUILDING WORKSHOP JOINTLY HOSTED BY THE MEDICAL COUNCIL OF MALAWI AND THE MINISTRY OF HEALTH

Harold Chintembo

BWB secures $145 million for operational improvements

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.