Nduna ya Zofalitsa nkhani, a Moses Kunkuyu, yayamika m’modzi mwa anthu ochita malonda pa luso la makono (ICT), a Wisely Phiri, amene ndi mwini wake wa Sparc Systems, kaamba komanga nyumba ya makono kwambiri munzinda wa Lilongwe.
A Kunkuyu ati zimene achita a Phiri ndi umboni okuti mu ntchito za ICT muli ndalama zimene zingathandize pa chitukuko cha dziko lino.
Iwo anati nthawi zambiri a Malawi amaziyang’anira pansi m’malo mochita zinthu zothandiza kutchukitsa dziko lino.
A Phiri anati alinso ndi mapulani omanga sukulu yophunzitsa ICT ku Blantyre komanso mayiko a Zambia ndi Mozambique.
Iwo apempha boma kuti lidzipereka ma contract ambiri kwa a business achi Malawi pofuna kulimbikitsa aMalawiwo pa ntchito zokweza dziko lino.
Sparc Systems Limited adayikhazikitsa 2013 ndipo ili ndi ofesi kuno ku Malawi, Zambia ndi Rwanda.