Phungu wa dera laku m’mwera kwa Msinja m’boma la Lilongwe, a Francis Belekanyama, wapempha achinyamata kuti asiye kudziyang’anira pansi pazochitika zokhudza ndale m’dziko muno.
A Belekanyama amayankhula izi pa msonkhano omwe unali pa bwalo lamasewero la Kambanizithe umene anaukonza ndi chofuna kulimbikitsa anthu kuti akalembetse mu kaundula wa zisankho za chaka cha mawa.
Iwo anati akuona kuti nthawi yakwana kuti nawo achinyamata adzikhala patsogolo pa ntchito zachitukuko komanso kukhala adindo pa ndale posankha adindo omwe angawatumikire moyenera.
Wapampando wa m’chipani cha Malawi Congress (MCP), a Patrick Zebron Chilondola, anathokoza a Belekanyama poika chidwi kwa anthu a m’dera lake ndipo anapemphanso aphungu ena kuti nawo adzichita motero.
Pamsonkhanowu panafikanso akuluakulu ndi aphungu osiyanasiyana achipani cha MCP kuphatikizapo nduna ya zachuma a Simplex Chithyola Banda.
Mwezi wa mawa, bungwe la Malawi Electoral Commission likhala likuyamba ntchito yolembetsa anthu amene akaponye voti pachisankho cha chaka cha mawa.