Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani

‘Tikusowekera chakudya, zipangizo zophunzitsira ntchito za manja’

M’busa Thomson John Chipeta, yemwe anakhazikitsa Home of Hope Orphanage, m’boma la Mchinji wati mabvuto akulu omwe akukumananawo ndi kuchepa kwa chakudya komanso zipangizo zophunzitsira ntchito za manja komanso luso pa malowa.

Iwo akusunga ana oposera 600, ndipo onsewa amaphunzira pa malowa omwe kaamba koti pali sukulu ya pulaimale, sekondale, komanso ya ntchito za manja komanso luso.

Iwo ati makina osokera komanso zipangizo zomphunzitsira ntchito ya zomangamanga, kuwotchelera komanso kupala matabwa ndi zosakwanira, akayelekeza ndi chiwerengero cha amene akuchita maphunziro amenewa.

Komabe ayamika makampani komanso anthu omwe akhala akupereka nthandizo losiyana siyana kuti ana asakhale ndi njala.

Pakadali pano, nduna yoona za chisamaliro cha anthu a Jean Sendeza yalamula DC wa boma la Mchinji kuti ayankhulane ndi akuluakulu a nthambi ya boma yoona ngozi zakugwa mwadzidzi ya DoDMA kuti lipereke chimanga kuti ana apamalowa asabvutike.

A Sendeza achenjezanso kuti boma litseka malo omwe akusunga ana amasiye akupeza kuti akuzunza komanso kuchitira ana nkhaza. Iwo ayamikira Home of Hope kaamba kowonetsetsa kuti ana akupatsidwa malo ogona okha, komaso zofunikira za tsiku ndi tsiku, kuphatikizirapo chisamaliro ndi uphungu oyenera okhudza moyo wa uzimu ndi maphunziro ena ofunikira pamene akukula.

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Police Officer dies in the line of duty

Charles Pensulo

Alimi apeza misika ya ndalama zochuluka kuchiwonetsero chazaulimi

Justin Mkweu

Dr Usi atsindika zakufunikira kwa mgwirizano

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.