Mwini wake wa kampani ya J.S Fitness ku Lilongwe, a Clement Udedi ati ndikofunika kuti aliyense atengepo gawo pothana ndi matenda a cancer ya m’mawere.
A Udedi anena izi pomwe anali ndi ulendo wa ndawala komanso majowajowa munzinda wa Lilongwe omwe cholinga chake chinali kudziwitsa anthu za matendawa komanso kufuna kutolera ndalama zothandizira chimodzi mwa zipatala zing’onozing’ono zomwe zili mbali yaku Airwing munzindawu.
“Ngati JS Fitness gym tinaganiza kuti ife tichitepo mbali yathu. Tayenda ndipo tafalitsa uthenga ndipo tikudziwa kuti winawake wathandizika,” anatero a Udedi.
Bungwe loyang’anira za umoyo pa dziko lonse lapansi la World Health linakhazikitsa mwezi wa October ngati okumbukira za matenda a cancer ya m’mawere padziko lonse.