Mabanja okwana makumi asanu ammudzi mwa mfumu yaikulu Masumbakhunda ozungulira khalango ya Dzalanyama m’boma la Lilongwe ali ndi chimwemwe atalandira mbaula zamakono zoyendera mphamvu ya dzuwa kuchokera ku bungwe la Save the Children.
Malinga ndi m’modzi mwa akuluakulu ku bungwel, a Bright Chidzumeni, kupereka mbaulazi ndi njira imodzi yochepetsa mavuto owononga nkhalango ya Dzalanyama, mmene anthu akhala akudulamo mitengo mopanda chilorezo ndicholinga chopanga nkhuni komanso makala ophikira.
M’modzi mwa anthu amene alandira nawo mbaulazi, a Lydia Banda, anati ithandiza kuchepetsa mchitidwe ogwiritsa ntchito ana kukafuna nkhuni ku nkhalangoyi popeza mbaulazi zimagwiritsa ntchito nkhuni zochepa.