Apolisi m’chigawo chakumwera kuzambwe agwila amayi awiri komanso bambo m’modzi chifukwa chopezeka ndi zinthu zaku nkhalango popanda chilolezo komanso kuzembetsa makala popanda zikalata zowayeneleza.
Malipoti omwe MBC yapeza asonyesa kuti komishonala wapolisi mchigawochi, a Noel Kaira, omwe anali limodzi
ndi maofesala awo kugwira ntchito yoyendera m’malo osiyanasiyana, usiku wa Lamulungu
anakumana ndi galimoto ya mtundu wa Scania pa roundabout ya Kameza.
Pokaikira zomwe inanyamula anayipanga chipikisheni ndipo anapeza kuti inali itadzadza ndi matumba a makala.
Apolisiwo anakwanitsa kugwira Samuel Ngwangwa, wochokera pamudzi wa Chaswatheka, T/A Kunthembwe m’boma lomwelo la Blantyre, yemwe ndi dalaivala wa loleyo, a Merenia Chimtanda, wochokera pamudzi wa Dzikolatha, T/A Mlauli, m’boma la Neno omwe amachita malonda komanso a Mary Thuboyi, wochokera pamudzi wa Chang’ambika, T/A Chapananga, m’boma la Chikwawa omwenso amachita bizinesi.
Kuyambira chaka, chatha apolisi alimbikitsa ntchito yoteteza zinthu zaku nkhalango pogwira limodzi ntchito ndi nthambi zosiyanasiyana, kuphatikizapo yaza nkhalango komanso yolimbana ndi mchitidwe wa ziphuphu ndi katangale ya Anti-Corruption Bureau.