Queens yagonja 65-35 ndi South Africa mu mpikisano wa m’mayiko a mu Africa umene ukuchitikira m’dziko la Namibia.
Malawi, yomwe inagonjetsa Zambia mu masewero ake oyamba, inatsalira m’zigawo zonse zinayi za masewerowo.
Apa ndiye kuti timuyi ili pa nambala yachiwiri mu Gulu A momwe mulinso ma timu a Kenya ndi Zambia.
Ma timu awiri omwe amalize pamwamba pa gululi apitilira mu ndime ya semifainolo.
Timuyi isewera masewero ake omaliza a m’magulu lachinayi lino pomwe ikumane ndi timu ya Kenya.
Olemba: Amin Mussa