Mtsogoleri wa dziko lino Dr Lazarus Chakwera wati ndiokhutira ndi momwe ikuyendera ntchito yokonzanso msewu wa M1.
Dr Chakwera anena zimenezi pa Mtengowanthenga pomwe analankhula kwa nantindi wa anthu amene asonkhana.
Dr Chakwera anati anaganiza zodutsa mu msewu wa M1 popita ku Mzuzu, kuti awone yekha ntchitoyo.
Iwo anatsimikiziranso anthu kuti ntchito yokonza dzikoli ili mkati, kuti mibadwo ikubwerayi idzakhale ndi dziko labwino, ndipo anayamika anthu aku Dowa chifukwa ndi olimbika pa ntchito.
Mtsogoleri wa dziko linoyu anati nkofunika kuti dziko la Malawi likhale lodzidalira osati lopempha pempha.
“Komanso tiyeni tisamalire ntchito zachitukuko zomwe tili nazo, osaononga ayi ” anatero Dr Chakwera.
Olemba: Isaac Jali