Malawi Broadcasting Corporation
Development Local Local News Nkhani

MCP yayamikira anthu aku Mangochi powakhulupilira

Wapampando wa chipani cha Malawi Congress (MCP) m’chigawo chapakati a Zebron Chilondola ayamikira anthu a m’boma la Mangochi kaamba kowonetsa chikhulupiliro mu chipanichi.

A Chilondola ati izi zili chomwechi anthu m’bomali atasankha khansala wa MCP pa chisankho chapadera chimene chinachitika sabata yatha.

Iwo anena zimenezi pa Mtengowanthenga m’boma la Dowa pamene mtsogoleri wa dziko lino Dr Lazarus Chakwera anayankhula kwa anthu.

Pamwambowo, a Asiyatu Chakwera, amene ndi m’modzi mwa makhansala a chipani cha Democratic Progressive (DPP) m’boma la Salima, achoka m’chipanicho ndipo alowa chipani cha MCP.

A Oscar Taulo, amene anali m’modzi othandiza ku chipani cha DPP pa malamulo, alowanso MCP.

Olemba: Isaac Jali

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

LL Police recovers stolen TV, nabs suspect

Romeo Umali

COURT TO RULE ON SATTAR’S ACCOUNTS

MBC Online

Bullets secure another partner

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.