Mtsogoleri wa dziko lino Dr Lazarus Chakwera, wati atsogoleri amipingo ali ndi ntchito yaikulu yothandiza kupititsa patsogolo ntchito zachitukuko m’dziko muno.
Dr Chakwera alankhula izi pamene anali nawo pamwambo wa mapemphero pa mpingo wa Monkey Bay Assemblies of God m’boma la Mangochi.
“Inu atsogoleri a mipingo ndi amene dziko likudalira pachitukuko. Kupatula utumiki, tikudaliranso inu kutenga gawo polimbikitsa asungwana kupita patsogolo ndi maphunziro awo,” iwo anatero.
Mtsogoleri wadziko linoyu, amene analinso pamodzi ndi Madam Monica Chakwera, walimbikitsa a Khristu onse a mpingowu kuti akhale olimbikitsa umodzi muzochita zawo.
Olemba: Owen Mavula