Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani

Perekani mauthenga achisankho mosakondera – MEC

Bungwe la Malawi  Electoral Commission (MEC) lalangiza anthu azisudzo omwe  amachita masewero pa radio za MBC   mdziko muno  kuti adzipereka mauthenga olimbikitsa anthu kuti adzatenge nawo gawo pa chisankho mosakondera.

Komishonala wa bungwe la MEC, a Francis Kasaira,  ndi omwe anena izi mu mzinda wa Blantyre potsegulira maphunziro a masiku awiri omwe bungwe la NICE Public Trust lakonzera azisudzowa pa  momwe angaperekere mauthenga okhudza chisankho cha chaka cha mawa kudzera mumasewero.

“Pamene tikuyandikira mu nthawi yachisankho nkofunika kuti anthu azisudzo adzipereka uthenga okhudza chisankhochi motsatira malamulo osati kupereka uthenga omwe ndi okondera munthu wina wake kapena chipani china chake.” Atero a Kasaira.

Pothilirapo ndemanga mkulu wa bodi ya NICE Public Trust,  Lingalireni Mihowa ati bungwe lawo ligwira ntchito kwambiri ndi anthu azisudzo pofalitsa uthenga okhudza chisankho chomwe chichitike chaka cha mawa mdziko muno.

Mmodzi wa anthu omwe amapanga sewero la Nzeru mkupangwa pa wailesi ya MBC, Rosemary Malipa wati maphunzirowa awathandiza kuti adzitha kupereka mauthenga olondolo okhudza chisankho.

Masewero odziwika bwino omwe amawulutsidwa pa wailesi ya MBC ndi sewero la Pamajiga, Sewero la Sabata Ino komanso Nzeru Nkupangwa.

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Zonse zili mchimake, yatero PP

Yamikani Simutowe

PRISAM, MARANATHA ACADEMY OFFER FULL SCHOLARSHIP TO BRIGHT NEEDY STUDENT

McDonald Chiwayula

Wanderers, Bullets in second-spot showdown

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.